Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo dengu limodzi linali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.
Mateyu 25:2 - Buku Lopatulika Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Asanu anali opusa ndipo asanu ena anali ochenjera. |
Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo dengu limodzi linali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?
Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.
Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife.
Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.