Mateyu 24:51 - Buku Lopatulika nadzamdula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nadzamdula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu achiphamaso. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adzamulanga koopsa ndipo adzamuyika kokhala anthu achiphamaso, kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.” |
Ochimwa a mu Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire?
Ichi ndi chogwera chako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; chifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama.
Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.
Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
mbuye wa kapolo uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati nadzamuika dera lake pamodzi ndi anthu osakhulupirira.
Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mutulutsidwa kunja.