ndipo ana oyamba a m'dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.
Mateyu 24:41 - Buku Lopatulika awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Azimai aŵiri adzakhala akusinja, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amayi awiri adzakhala akusinja pa mtondo; wina adzatengedwa ndi wina adzatsala. |
ndipo ana oyamba a m'dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.
Tenga mipero, nupere ufa; chotsa chophimba chako, vula chofunda, kwinda m'mwendo, oloka mitsinje.
Munthu asalandire chikole mphero, ngakhale mwanamphero, popeza alandirapo chikole moyo wa munthu.