Mkuyu utchetsa nkhuyu zake zosakhwima, mipesa niphuka, inunkhira bwino. Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.
Mateyu 24:32 - Buku Lopatulika Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Yang'anani mkuyu kuti mutengerepo phunziro. Mukamaona kuti nthambi zake zayamba kukhala zanthete, ndipo masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsopano kuchokera ku mtengo wamkuyu phunzirani ichi: Pamene uyamba kuphukira, masamba ake akatuluka, mumadziwa kuti dzinja layandikira. |
Mkuyu utchetsa nkhuyu zake zosakhwima, mipesa niphuka, inunkhira bwino. Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.
Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.
chomwechonso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo.