Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwake munthu asatuluke m'malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri.
Mateyu 24:20 - Buku Lopatulika Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusakhale pa nyengo yachisanu, kapena pa Sabata; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusakhale pa nyengo yachisanu, kapena pa Sabata; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pempherani kuti nthaŵi pamene muzidzathaŵa, isadzakhale nyengo yachisanu, kapena pa tsiku la Sabata. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzachitike nthawi yozizira kapena pa Sabata. |
Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwake munthu asatuluke m'malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri.
pakuti pomwepo padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.
Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kuchokera kuphiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku la Sabata.