Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.
Mateyu 24:17 - Buku Lopatulika iye ali pamwamba pa tsindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 iye ali pamwamba pa chindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amene ali padenga pa nyumba yake, asatsike nkuloŵanso m'nyumba mwake kuti akatenge katundu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yemwe ali pa denga la nyumba yake asatsike kukatulutsa chinthu chilichonse mʼnyumba. |
Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.
Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.
Chimene ndikuuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m'khutu, muchilalikire pa matsindwi a nyumba.
Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?
Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati chidzalalikidwa pa matsindwi a nyumba.
Ndipo posapeza polowa naye, chifukwa cha unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa tsindwi, namtsitsira iye poboola pa tsindwi ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.
Koma m'mawa mwake, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mzinda, Petro anakwera patsindwi kukapemphera, ngati pa ora lachisanu ndi chimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya;
Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lake, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.
Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumzinda, iye anakamba ndi Saulo pamwamba pa nyumba yake.