Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.
Mateyu 24:13 - Buku Lopatulika Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero koma wopirira kufikira chimaliziro adzapulumuka. |
Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.
Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusaweruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala.
Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.
Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa: koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa.
Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.
kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;
amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira chimaliziro, kuti mukhale opanda chifukwa m'tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.
Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.
pakuti takhala ife olandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro;
koma Khristu monga mwana, wosunga nyumba yake; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa chiyembekezocho, kuchigwira kufikira chitsiriziro.
Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.