Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.
Mateyu 24:10 - Buku Lopatulika Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa nthaŵi imeneyo ambiri adzataya chikhulupiriro chao, azidzaperekana nkumadana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi imeneyo ambiri adzasiya chikhulupiriro ndipo adzadana ndi kuperekana wina ndi mnzake, |
Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.
ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo.
Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake.
Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuti amuphe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzayambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa.
ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mau, pomwepo akhumudwa.
Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a fuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani.
Ichi uchidziwa, kuti onse a mu Asiya adabwerera kusiyana nane; a iwo ali Figelo ndi Heremogene.
pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.
Pa chodzikanira changa choyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; chimenecho chisawerengedwe chowatsutsa.