Mateyu 23:23 - Buku Lopatulika Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumapereka chakhumi cha timbewu tonunkhira ndi cha timbewu tokometsera chakudya. Koma mwasiya zofunikira kwambiri za mʼmalamulo monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. Muyenera kuchita zomalizirazi komanso osasiya zoyambazo. |
Atakonza thyathyathya pamwamba pake, kodi safesa ponse mawere, ndi kumwazamwaza chitowe, nafesa tirigu m'mizere ndi barele m'malo ake osankhika, ndi mchewere m'maliremo?
Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano.
Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.
Limodzi mwa magawo khumi la zonse m'dziko, la mbeu zake za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova.
Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.
Koma mukadadziwa nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; simukadaweruza olakwa iwo osachimwa,
Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.
Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadze kudzaitana olungama, koma ochimwa.
Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.
ndisala chakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndili nazo.
Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.