Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo Inu nthawi zosatha.
Mateyu 23:21 - Buku Lopatulika Ndipo wakulumbira kutchula Kachisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wakulumbira kutchula Kachisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, walumbiranso pa zonse zimene zili m'Nyumbamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo iye wolumbira potchula Nyumba ya Mulungu alumbira pa Nyumbayo ndi pa Iye amene amakhala mʼmenemo. |
Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo Inu nthawi zosatha.
Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.
Ndipo ansembe sanakhoze kulowa m'nyumba ya Yehova, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.
Chifukwa chake wakulumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pake.