Mateyu 23:12 - Buku Lopatulika Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo amene aliyense akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa. |
Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.
Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.
Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.
Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.
Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;