Mateyu 23:11 - Buku Lopatulika Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakati panupa wamkulu akhale mtumiki wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wamkulu pakati panu adzakhala wokutumikirani. |
Ndipo m'mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.
Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka.
Kodi ali atumiki a Khristu? (Ndilankhula monga moyaluka), makamaka ine; m'zivutinso mochulukira, m'ndende mochulukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawirikawiri.
Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu.
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.