Mateyu 22:43 - Buku Lopatulika Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amtchula Iye bwanji Ambuye, nanena, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amtchula Iye bwanji Ambuye, nanena, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye adaŵafunsa kuti, “Tsono bwanji nanga Davideyo ndi nzeru zochokera kwa Mzimu Woyera, akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake? Paja adati, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anawawuza kuti, “Nanga zikutheka bwanji kuti Davide poyankhula mwa Mzimu Woyera amatchula Iye ‘Ambuye?’ Pakuti akuti, |
Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.
Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.
Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.
pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.
Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,
Pomwepo ndinakhala mwa Mzimu; ndipo, taonani padaikika mpando wachifumu mu Mwamba ndi pa mpandowo padakhala wina;