Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;
Mateyu 22:42 - Buku Lopatulika nati, Muganiza bwanji za Khristu? Ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nati, Muganiza bwanji za Khristu? Ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adati, “Mumaganiza chiyani za Mpulumutsi wolonjezedwa uja? Mumati ndi mwana wa yani?” Iwo aja adati, “Ndi mwana wa Davide.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Kodi mukuganiza bwanji za Khristu? Ndi Mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti, “Mwana wa Davide.” |
Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;
Ndipo iwo amene anali m'ngalawamo anamgwadira, nanena, Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!
Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.
pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.