nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwake adzakwatira mkazi wake, nadzamuukitsira mbale wake mbeu.
Mateyu 22:25 - Buku Lopatulika Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwake mkazi wake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwake mkazi wake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono kwathu kudaali anthu asanu ndi aŵiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, nkumwalira. Tsono popeza kuti analibe mwana, adasiyira mbale wake mkazi wake uja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo. |
nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwake adzakwatira mkazi wake, nadzamuukitsira mbale wake mbeu.