Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Mateyu 22:22 - Buku Lopatulika Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nachokapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nachokapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamva zimenezi, anthuwo adathedwa nzeru, motero adamsiya nachokapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atamva izi, anadabwa, ndipo anamusiya Iye, nachoka. |
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.
Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka.
Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.
Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.