Iye anavomera, Apereka. Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja?
Mateyu 22:19 - Buku Lopatulika Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo anadza nalo kwa Iye rupiya latheka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo anadza nalo kwa Iye rupiya latheka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tandiwonetsani ndalama yamsonkho.” Iwo adampatsadi ndalamayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onetseni ndalama imene mumapereka msonkho.” Iwo anabweretsa dinari, |
Iye anavomera, Apereka. Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja?
Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola.
Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake.
Ndipo ananena nao, Chithunzithunzi ichi, ndi chilembo chake zili za yani? Ndipo anati kwa Iye, Za Kaisara,
Ndipo ndinamva ngati mau pakati pa zamoyo zinai, nanena, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; ndi mafuta ndi vinyo usaziipse.