Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mzinda uwu ndi kutsiriza malinga ake, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m'njira; ndipo potsiriza pake kudzasowetsa mafumu.
Mateyu 22:17 - Buku Lopatulika Chifukwa chake mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye timati mutiwuze zimene mukuganiza. Kodi Malamulo a Mulungu amatilola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tiwuzeni tsono maganizo anu ndi otani, kodi nʼkololedwa kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” |
Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mzinda uwu ndi kutsiriza malinga ake, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m'njira; ndipo potsiriza pake kudzasowetsa mafumu.
Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa aliyense wa ansembe, ndi Alevi, oimbira, odikira, antchito a m'kachisi, kapena antchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira.
Panali enanso akuti, Takongola ndalama za msonkho wa mfumu; taperekapo chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.
Ndipo lichulukitsira mafumu zipatso zake, ndiwo amene munawaika atiweruze, chifukwa cha zoipa zathu; achitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zoweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukulu.
Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzachita.
Iye anavomera, Apereka. Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja?
Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linatuluka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe;
Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;
amene Yasoni walandira; ndipo onsewo achita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu ina, Yesu.
koma Paulo podzikanira ananena, Sindinachimwe kanthu kapena pachilamulo cha Chiyuda, kapena pa Kachisi, kapena pa Kaisara.
Koma tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponseponse.
Atapita ameneyo, anauka Yudasi wa ku Galileya, masiku a kalembera, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.