Mateyu 22:14 - Buku Lopatulika Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo owerengeka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo owerengeka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adati, “Inde oitanidwa ngambiri, komatu osankhidwa ngoŵerengeka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Popeza oyitanidwa ndi ambiri koma osankhidwa ndi ochepa.” |
Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.
chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.
Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse;
Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawagonjetsa, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.