Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.
Mateyu 21:6 - Buku Lopatulika Ndipo ophunzirawo anamuka, nachita monga Yesu anawauza; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ophunzirawo anamuka, nachita monga Yesu anawauza; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ophunzira aja adapitadi nakachita monga momwe Yesu adaaŵalamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzirawo anapita nachita monga Yesu anawalamulira. |
Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.
Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.
Ndipo ndinachita monga momwe anandilamulira, ndinatulutsa akatundu anga usana, ngati a pa ulendo wa kundende, ndi madzulo ndinaboola pakhoma ndi dzanja langa, ndinawatulutsa pali mdima, ndi kuwasenza paphewa panga pamaso pao.
Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.
Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.