Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Mateyu 21:4 - Buku Lopatulika Ndipo ichi chinatero, kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ichi chinatero, kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimenezi zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri adaanena kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Izi zinachitika kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri: |
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,
Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza.
Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.
Ndipo anabwera naye mwana wa bulu kwa Yesu, naika zovala zao pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo.
Ndipo anadza naye kwa Yesu; ndipo anayalika zovala zao pa mwana wa buluyo, nakwezapo Yesu.
M'mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu,