Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira.
Mateyu 21:22 - Buku Lopatulika Ndipo zinthu zilizonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo zinthu zilizonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati mukhala ndi chikhulupiriro, zonse zimene mungapemphe kwa Mulungu mudzalandira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.” |
Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira.
Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu zilizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.
Ndipo chimene chilichonse mukafunse m'dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana.
Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.
Kufikira tsopano simunapemphe kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.
ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.