Nyengo imeneyo Yesu anapita tsiku la Sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake anali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya.
Mateyu 21:18 - Buku Lopatulika Ndipo mamawa, m'mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mamawa, m'mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, pamene Yesu ankabwerera ku Yerusalemu, adaamva njala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmamawa, pamene amabwera ku mzinda, anamva njala. |
Nyengo imeneyo Yesu anapita tsiku la Sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake anali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya.
Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala.
kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai. Ndipo Iye sanadye kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.
Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.