M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu, chifukwa cha otsutsana ndi Inu, kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.
Mateyu 21:16 - Buku Lopatulika nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa nafunsa Yesu kuti, “Kodi mukumva zimene akunenazi?” Yesu adaŵayankha kuti, “Inde. Kani simudaŵerenge konse mau a Mulungu aja akuti, ‘Mudaphunzitsa ana ndi makanda omwe kukutamandani kotheratu?’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anamufunsa kuti, “Kodi mukumva zimene anawa akunena?” Yesu anayankha nati, “Inde. Kodi simunawerenge kuti, “Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda mwatuluka mayamiko?” |
M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu, chifukwa cha otsutsana ndi Inu, kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.
Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:
Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenge chimene anachichita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye?
Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi,
Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenge kodi chomwe chinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,
Ndipo ananena nao, Simunawerenge konse chimene anachichita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye?
Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! Pakuti padzakhala chisauko chachikulu padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.