Mateyu 21:14 - Buku Lopatulika Ndipo anadza kwa Iye ku Kachisiko akhungu ndi opunduka miyendo, nachiritsidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadza kwa Iye ku Kachisiko akhungu ndi opunduka miyendo, nachiritsidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu akhungu ndi opunduka adadza kwa Yesu m'Nyumba ya Mulungumo, ndipo Iye adaŵachiritsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu osaona ndi olumala anabwera kwa Iye mʼNyumba ya Mulungu ndipo anawachiritsa. |
Koma ansembe aakulu ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,
Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.
Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.