Mboni zanu zivomerezeka ndithu; chiyero chiyenera nyumba yanu, Yehova, kunthawi za muyaya.
Mateyu 21:13 - Buku Lopatulika nanena kwa iwo, Chalembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena kwa iwo, Chalembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.” |
Mboni zanu zivomerezeka ndithu; chiyero chiyenera nyumba yanu, Yehova, kunthawi za muyaya.
naonso ndidzanka nao kuphiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa paguwa langa la nsembe; pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.
Kodi nyumba ino, imene itchedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndachiona, ati Yehova.
Ndipo anamuuza iye, Mu Betelehemu wa Yudeya; chifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti,
Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.
Kwalembedwa, Ndipo nyumba yanga idzakhala nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.
Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.