Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 20:6 - Buku Lopatulika

Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse chabe?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse chabe?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pafupi 5 koloko madzulo adapitanso nakapeza enanso akungokhala. Adaŵafunsa kuti, ‘Bwanji mwangokhala khale pano tsiku lonse osagwira ntchito?’

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’

Onani mutuwo



Mateyu 20:6
10 Mawu Ofanana  

Ulesi ugonetsa tulo tofa nato; ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.


Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Taona, mphulupulu ya mng'ono wako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kuchuluka kwa chakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ake; ndipo sanalimbitse dzanja la wosauka ndi wosowa.


Ndiponso anatuluka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nachita chimodzimodzi.


Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa.


Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu aliyense rupiya latheka limodzi.


Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.


(Koma Aatene onse ndi alendo akukhalamo anakhalitsa nthawi zao, osachita kanthu kena koma kunena kapena kumva cha tsopano.)


kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.