Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.
Mateyu 20:27 - Buku Lopatulika ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyamba akhale kapolo wanu. |
Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.
Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;
monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.
Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.
Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?
Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu.