Mateyu 20:16 - Buku Lopatulika Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adati, “Choncho amene ali oyambirira adzakhala otsirizira. Ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Momwemo omalizira adzakhala oyamba ndipo oyamba adzakhala omalizira.” |
Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.
Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho.
Pakuti ndinena kwa inu, kuti kulibe mmodzi wa amuna oitanidwa aja adzalawa phwando langa.
Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.
Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono.
Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa;
ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero.
Chifukwa chake tidzatani? Kuti amitundu amene sanatsate chilungamo, anafikira chilungamo, ndicho chilungamo cha chikhulupiriro;
Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandire monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.