Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'galeta wake.
Mateyu 20:14 - Buku Lopatulika Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tenga malipiro ako, uzipita. Mwiniwakene ndafuna kuti ndipatse wolembedwa potsirizayu molingana ndi iwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe. |
Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'galeta wake.
Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangane ndi ine pa rupiya latheka limodzi?
Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?
Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alinkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
Koma iye ananena naye, Mwana wanga, iwe uli ndine nthawi zonse, ndipo zanga zonse zili zako.
Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.
monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha.
Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;
Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndipo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa, Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu, ndi kuti mukapambane m'mene muweruzidwa.