Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.
Mateyu 20:12 - Buku Lopatulika nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa adati, ‘Aa! Anzathu otsiriziraŵa angogwira ntchito kanthaŵi pang'ono, bwanji mwaŵapatsa malipiro olingana ndi athu, pamene ifeyo tathyoka nayo ntchito tsiku lathunthu, ndi chidzuŵa chonse chija?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’ |
Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.
Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.
Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa chabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wake, ndi kuyenda ovala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu?
Ndipo pamene mphepo ya kumwera iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.
Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La ntchito kodi? Iai; koma ndi lamulo la chikhulupiriro.
ngatitu ndiye Mulungu mmodzi, amene adzawayesa amdulidwe olungama ndi chikhulupiriro, ndi akusadulidwa mwa chikhulupiriro.
Kufikira nthawi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika;
kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino,
Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake.