Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;
Mateyu 2:17 - Buku Lopatulika Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo zidachitikadi zimene mneneri Yeremiya adaanena kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo, zimene ananena mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa: |
Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;
nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito.
Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.
Mau anamveka mu Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo.
Pamenepo chinakwaniridwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, ndi kuti, Ndipo iwo anatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu, mtengo wa uja wowerengedwa mtengo wake, amene iwo a ana a Israele anawerenga mtengo wake;