Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israele.
Mateyu 2:15 - Buku Lopatulika nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke m'Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira, kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Ndidaitana Mwana wanga kuti atuluke ku Ejipito.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero nakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira. Ndipo zinakwaniritsidwa zomwe ananena Ambuye mwa mneneri kuti, “Ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.” |
Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israele.
Mulungu amtulutsa mu Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake.
Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,
Koma pakumwalira Herode, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera m'kulota kwa Yosefe mu Ejipito,
nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.
Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.
kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Iye yekha anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu.
Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.
Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu.
Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.