Mateyu 19:20 - Buku Lopatulika Mnyamatayo ananena kwa Iye, Zonsezi ndinazisunga, ndisowanso chiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mnyamatayo ananena kwa Iye, Zonsezi ndinazisunga, ndisowanso chiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu uja adati, “Malamulo onseŵa ndakhala ndikuŵatsata, nanga chanditsaliranso nchiyani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mnyamatayo anati, “Zonsezi ndimazisunga, nanga chatsala ndi chiyani?” |
Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.
Koma anayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwire lamulo lanu nthawi iliyonse; ndipo simunandipatse ine kamodzi konse mwanawambuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga.
Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.
Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe Iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala.
Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.
Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro.
monga mwa changu, wolondalonda Mpingo; monga mwa chilungamo cha m'lamulo wokhala wosalakwa ine.