Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.
Mateyu 19:13 - Buku Lopatulika Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ena ankabwera ndi ana kuti Yesu aŵasanjike manja ndi kuŵapempherera, ophunzira ake nkumaŵazazira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo anabwera nawo ana kwa Yesu kuti awasanjike manja ndi kuwapempherera. Koma ophunzira ake anadzudzula amene anabweretsa anawo. |
Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.
ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;
Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ai.
Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m'mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire.
Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide.
Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.
Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.
Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.