Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.
Mateyu 19:11 - Buku Lopatulika Koma Iye anati kwa iwo, Onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Iye anati kwa iwo, Onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaŵauza kuti, “Si anthu onse angamvetse zimenezi ai, koma okhawo amene Mulungu aŵathandiza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Si aliyense amene angavomere chiphunzitso ichi, koma kwa okhawo amene achimvetsetsa. |
Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.
Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira.
Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m'mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire.
Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika mu Mipingo yonse.
Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.
Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa.