Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.
Mateyu 19:10 - Buku Lopatulika Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira ake adamuuza kuti, “Ndiyetu ngati zili choncho pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, ndi bwino tsono kusakwatira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira ake anati kwa Iye, “Ngati umu ndi mmene zilili pa mwamuna ndi mkazi, kuli bwino kusakwatira.” |
Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.
Koma Iye anati kwa iwo, Onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa.
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.
Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.
a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.