Pamenepo kapolo mnzakeyu anagwada pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera.
Mateyu 18:26 - Buku Lopatulika Chifukwa chake kapoloyo anagwada pansi, nampembedzera, nati, Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake kapoloyo anagwada pansi, nampembedzera, nati, Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo wantchito uja adamgwadira nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani ndithu zonse.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Wantchitoyo anagwada pamaso pake namupempha iye kuti, ‘Lezereni mtima ndipo ndidzabweza zonse.’ |
Pamenepo kapolo mnzakeyu anagwada pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera.
Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.
Ndipo onani, wakhate anadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.
Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonje ku chilungamo cha Mulungu.