Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.
Mateyu 18:25 - Buku Lopatulika Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wake analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wake analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye popeza kuti adaasoŵa chobwezera ngongoleyo, mbuye wake uja adalamula kuti amgulitse wantchitoyo pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake ndi zake zonse, kuti ngongole ija ibwezedwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Popeza sakanatha kubweza, bwanayo analamula kuti iye, mkazi wake, ana ake ndi zonse anali nazo zigulitsidwe kuti zibweze ngongoleyo. |
Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.
Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu aamuna ndi aakazi akhale akapolo, ndi ana athu aakazi ena tawatengetsa kale; ndipo tilibe ife mphamvu ya kuchitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena.
Ndipo ndinanena nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala duu, nasowa ponena.
Ukagula mnyamata Muhebri, azigwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi; koma chachisanu ndi chiwiri azituluka waufulu chabe.
Litamtulukira dzuwa, pali chamwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wake.
Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.
Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi kudzigulitsa kwa iwe; usamamgwiritsa ntchito monga kapolo;
Ndipo pamene anayamba kuwerengera, anadza kwa iye ndi wina wamangawa wa ndalama za matalente zikwi khumi.
Popeza analibe chobwezera iwo, anawakhululukira onse awiri. Chotero, ndani wa iwo adzaposa kumkonda?