Mateyu 18:19 - Buku Lopatulika Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Komanso ndikukuwuzani inu kuti ngati awiri a inu pa dziko lapansi avomerezana kanthu kalikonse kamene mukapempha, Atate anga akumwamba adzakuchitirani. |
usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu zilizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.
Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.
Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.
Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa.
Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.
Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Mpingo anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.
Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kutulukira kunka ku Masedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.
Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;
ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.