Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga padziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula padziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba.
Mateyu 18:18 - Buku Lopatulika Indetu ndinena kwa inu, Zilizonse mukazimanga padziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo zilizonse mukazimasula padziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Indetu ndinena kwa inu, Zilizonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo zilizonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mudzamanga pansi pano, chidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo chilichonse chimene mudzamasula pansi pano, chidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti chilichonse chimene muchimanga pa dziko lapansi, chidzamangidwanso kumwamba, ndipo chilichonse chimene muchimasula pa dziko chidzamasulidwanso kumwamba. |
Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga padziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula padziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba.
Zochimwa za anthu ali onse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.
Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu, pamaso pa Khristu;