Mateyu 18:13 - Buku Lopatulika Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithu ndikunenetsa kuti ataipeza, chimwemwe chake chokondwerera imeneyo chimapambana chokondwerera zina zija zimene sizidatayike. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti akayipeza amasangalala kwambiri chifukwa cha nkhosa imodziyo kuposa nkhosa 99 zimene sizinasochere. |
Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.
Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako aamuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.
Zofooka simunazilimbitse; yodwala simunaichiritse, yothyoka simunailukire chika, yopirikitsidwa simunaibweze, yotayika simunaifune; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa.
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.
Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.
Nanga muyesa bwanji? Ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo?
Chomwecho sichili chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike.
Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.