Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.
Mateyu 17:19 - Buku Lopatulika Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoze bwanji kuchitulutsa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoza bwanji kuchitulutsa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake ophunzira aja adadza kwa Yesu paseri namufunsa kuti, “Ifeyo ndiye tinalephera bwanji kuutulutsa mzimu woipa uja?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo ophunzira anabwera kwa Yesu mwamseri ndi kumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwandacho?” |
Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.
Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.
Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo.
Ndipo pamene Iye adalowa m'nyumba, ophunzira ake anamfunsa m'tseri, kuti, Nanga bwanji sitinathe ife kuutulutsa?