Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi.
Mateyu 17:16 - Buku Lopatulika Ndipo ndinadza naye kwa ophunzira anu, koma iwo sanathe kumchiritsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinadza naye kwa ophunzira anu, koma iwo sanathe kumchiritsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndinabwera naye kwa ophunzira anuŵa, koma alephera kumchiritsa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndinabwera naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.” |
Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi.
Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno.
Ndipo pa chikhulupiriro cha m'dzina lake dzina lakelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo chikhulupiriro chili mwa Iye chinampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.