Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.
Mateyu 17:15 - Buku Lopatulika Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala nkhunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adati, “Ambuye mchitireni chifundo mwana wanga. Ali ndi khunyu ndipo amavutika koopsa. Kaŵirikaŵiri amagwa pa moto mwinanso m'madzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati, “Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi. |
Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.
Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Koma Yudasinso amene akampereka Iye, anadziwa malowa; chifukwa Yesu akankako kawirikawiri ndi ophunzira ake.