Mateyu 17:14 - Buku Lopatulika Ndipo pamene iwo anadza kukhamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene iwo anadza kukhamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene iwo adafikanso kumene kunali khamu la anthu kuja, munthu wina adadzagwadira Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atafika ku gulu la anthu, munthu wina anamuyandikira Yesu ndi kugwada pamaso pake. |
Ndipo anadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza.
Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?
Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,