Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.
Mateyu 17:11 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anayankha, nati, Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anayankha, nati, Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Inde Eliya ayambadi wabwera nkudzakonzanso zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Kunena zoona, Eliya adzayenera kubwera ndipo adzakonza zinthu zonse. |
Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.
Ndipo ophunzira ake anamfunsa, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza?
koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwe iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi iwo.
Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa Iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi ino mubwezera ufumu kwa Israele?
amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.