Mateyu 17:10 - Buku Lopatulika Ndipo ophunzira ake anamfunsa, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ophunzira ake anamfunsa, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira aja adamufunsa kuti, “Nanga bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Eliya adzayenera kuyamba wabwera?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira anamufunsa Iye kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kukhala woyamba kubwera?” |
Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.
Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.
Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?