Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.
Mateyu 16:4 - Buku Lopatulika Obadwa oipa ndi achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona. Ndipo Iye anawasiya, nachokapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Obadwa oipa ndi achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona. Ndipo Iye anawasiya, nachokapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu a mbadwo woipa ndi wosakhulupirika amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzaona chizindikiro china kupatula chokha chija cha mneneri Yona.” Atatero, Yesu adaŵasiya nachokapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mʼbado woyipa ndi wachigololo umafuna chizindikiro chodabwitsa koma palibe ngakhale chimodzi chidzapatsidwa kupatula chizindikiro cha Yona.” Pamenepo Yesu anawasiya nachoka. |
Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.
Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwachokera.
Koma Yehova anaikiratu chinsomba chachikulu chimeze Yona; ndipo Yona anali m'mimba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku.
Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.
Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno!
Pakuti yense wakuchita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mau anga mu mbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ake oyera, mu ulemerero wa Atate wake.
Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.
Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.