Pakuti ukakhala chete konse tsopano lino, chithandizo ndi chipulumutso kwa Ayuda zidzafuma kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate wako mudzaonongeka; ndipo kaya, kapena walowera ufumu chifukwa cha nyengo yonga iyi.
Mateyu 16:25 - Buku Lopatulika Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza. |
Pakuti ukakhala chete konse tsopano lino, chithandizo ndi chipulumutso kwa Ayuda zidzafuma kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate wako mudzaonongeka; ndipo kaya, kapena walowera ufumu chifukwa cha nyengo yonga iyi.
Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka mu Susa, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke.
Iye amene apeza moyo wake, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzaupeza.
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
Pakuti yense wakufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya; ndipo yense wakutaya moyo wake chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.
Iye aliyense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye aliyense akautaya, adzausunga.
Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m'dziko lino lapansi adzausungira kumoyo wosatha.
Ndipo iwo anampambana iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonde moyo wao kungakhale kufikira imfa.